44 Kuwonjezera apo, Yehova anawapatsa mpumulo+ pakati pa adani awo onse owazungulira, mogwirizana ndi zonse zimene analumbirira+ makolo awo. Panalibe ngakhale mdani mmodzi pa adani awo onse amene anatha kulimbana nawo.+ Yehova anapereka adani awo onse m’manja mwawo.+