-
Yoswa 13:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 (Dera loyambira kukamtsinje kotuluka mu Nailo kum’mawa kwa Iguputo, kukafika kumpoto kumalire ndi Ekironi,+ ankalitcha dziko la Akanani.)+ Madera a Afilisitiwa akulamulidwa ndi olamulira ogwirizana asanu.+ Maderawo ndi Gaza,+ Asidodi,+ Asikeloni,+ Gati+ ndi Ekironi,+ komanso Aavi+ akukhala komweko.
-
-
1 Mafumu 8:65Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
65 Pa nthawi imeneyo Solomo anachita chikondwerero+ pamodzi ndi Aisiraeli onse. Unali mpingo waukulu+ wa anthu amene anachokera kumadera osiyanasiyana, kuyambira polowera ku Hamati+ n’kutsetsereka mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+ Anachita chikondwererochi pamaso pa Yehova Mulungu wathu masiku 7, ndi masiku enanso 7.+ Onse pamodzi masiku 14.
-