7 Choncho anasankha mizinda ina kuti ikhale yopatulika. Mizinda yake inali Kedesi+ ku Galileya m’dera lamapiri la Nafitali, Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, Kiriyati-ariba,+ kutanthauza Heburoni, m’dera lamapiri la Yuda.
24Ndiyeno Yoswa anasonkhanitsa pamodzi mafuko onse a Isiraeli ku Sekemu.+ Iye anaitanitsa akulu a Isiraeli,+ atsogoleri, oweruza, ndi akapitawo, ndipo iwo anaima pamaso pa Mulungu woona.+
67 Chotero anawapatsa mzinda wothawirako wa Sekemu+ ndi malo ake odyetserako ziweto m’dera lamapiri la Efuraimu, mzinda wa Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto,