Genesis 34:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Koma ana a Yakobo anabwerako kubusa kuja atangomva za nkhaniyi. Nkhaniyi inawapweteketsa mtima kwambiri ndipo anakwiya koopsa,+ pakuti Sekemu anachitira Isiraeli chinthu chonyazitsa kwambiri pogona ndi mwana wa Yakobo.+ Zimenezi zinali zosayenera kuchitika m’pang’ono pomwe.+ Oweruza 19:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Pamenepo mwini nyumbayo anatuluka ndi kuwauza kuti:+ “Iyayi abale anga,+ chonde, musachite choipa chilichonse, chifukwa munthuyu wabwera m’nyumba yanga. Musachite chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi ngati chimenechi.+ Oweruza 19:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Koma amunawo sanafune kumumvera, moti Mleviyo anatenga mdzakazi wake+ ndi kum’pereka kwa amunawo kunja. Pamenepo, anthuwo anayamba kumugona,+ ndipo anapitiriza kum’zunza+ usiku wonse mpaka m’mawa. M’bandakucha anamusiya kuti apite. 2 Samueli 13:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Koma Tamara anamuuza kuti: “Ayi, m’bale wanga! Usandichititse manyazi,+ chifukwa zimenezi n’zachilendo mu Isiraeli.+ Usachite chinthu chopusa, chochititsa manyazi ngati chimenechi.+
7 Koma ana a Yakobo anabwerako kubusa kuja atangomva za nkhaniyi. Nkhaniyi inawapweteketsa mtima kwambiri ndipo anakwiya koopsa,+ pakuti Sekemu anachitira Isiraeli chinthu chonyazitsa kwambiri pogona ndi mwana wa Yakobo.+ Zimenezi zinali zosayenera kuchitika m’pang’ono pomwe.+
23 Pamenepo mwini nyumbayo anatuluka ndi kuwauza kuti:+ “Iyayi abale anga,+ chonde, musachite choipa chilichonse, chifukwa munthuyu wabwera m’nyumba yanga. Musachite chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi ngati chimenechi.+
25 Koma amunawo sanafune kumumvera, moti Mleviyo anatenga mdzakazi wake+ ndi kum’pereka kwa amunawo kunja. Pamenepo, anthuwo anayamba kumugona,+ ndipo anapitiriza kum’zunza+ usiku wonse mpaka m’mawa. M’bandakucha anamusiya kuti apite.
12 Koma Tamara anamuuza kuti: “Ayi, m’bale wanga! Usandichititse manyazi,+ chifukwa zimenezi n’zachilendo mu Isiraeli.+ Usachite chinthu chopusa, chochititsa manyazi ngati chimenechi.+