Levitiko 5:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 “‘Munthu akalumbira mpaka kulankhula mosalingalira bwino,+ mwa kunena kuti achita choipa+ kapena chabwino, ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake, koma akadziwa kuti walankhula mosalingalira bwino pa chilichonse chimene walumbira,+ pamenepo wapalamula mlandu pa chimene walumbiracho. Levitiko 19:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Musamalumbire zabodza m’dzina langa+ ndi kuipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova. Salimo 15:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+Koma anthu oopa Yehova amawalemekeza.+Akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.+ Mateyu 5:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire+ koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’+
4 “‘Munthu akalumbira mpaka kulankhula mosalingalira bwino,+ mwa kunena kuti achita choipa+ kapena chabwino, ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake, koma akadziwa kuti walankhula mosalingalira bwino pa chilichonse chimene walumbira,+ pamenepo wapalamula mlandu pa chimene walumbiracho.
4 Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+Koma anthu oopa Yehova amawalemekeza.+Akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.+
33 “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire+ koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’+