21 Kuwonjezera apo, pa nthawiyo Yoswa anapita n’kukafafaniziratu Aanaki.+ Aanakiwo anali kukhala kudera lamapiri, ku Heburoni, ku Debiri, ku Anabi,+ kudera lonse lamapiri la Yuda ndiponso kudera lonse lamapiri la Isiraeli.+ Yoswa anafafaniziratu Aanakiwo pamodzi ndi mizinda yawo.+