11 Kumeneko ukamvetsere zolankhula zawo.+ Pambuyo pake udzalimba mtima+ ndipo udzapitadi kumsasawo ndi kuuthira nkhondo.” Pamenepo, Gidiyoni ndi Pura mtumiki wake, anapita kumunsi pafupi kwambiri ndi asilikali amene anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo amene anali mumsasawo.