15 Pamenepo kamtengo kamingako kanauza mitengoyo kuti, ‘Ngati mukunenadi zoona kuti mukufuna kundidzoza kuti ndikhale mfumu, bwerani mubisale mumthunzi wanga.+ Koma ngati si choncho, moto+ utuluke mwa ine ndi kunyeketsa mikungudza+ ya ku Lebanoni.’+
20 Koma ngati si choncho, moto+ utuluke mwa Abimeleki ndi kunyeketsa nzika za Sekemu ndi anthu a m’nyumba ya Milo,+ komanso moto+ utuluke mwa nzika za Sekemu ndi anthu a m’nyumba ya Milo ndi kunyeketsa Abimeleki.”+