49 Chotero anthu onsewo, aliyense wa iwo anadula nthambi yake ndi kutsatira Abimeleki. Kenako anatsamiritsa nthambizo pachipinda chotetezekacho n’kuchiyatsa moto, moti nawonso anthu onse okhala munsanja ya Sekemu, amuna ndi akazi pafupifupi 1,000, anafa.+