-
2 Mafumu 14:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Yehoasi mfumu ya Isiraeli itamva inamuyankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti: “Chitsamba chaminga cha ku Lebanoni chinatumiza uthenga kwa mtengo wa mkungudza+ wa ku Lebanoni, wakuti, ‘Ndipatse mwana wako wamkazi kuti mwana wanga wamwamuna amukwatire.’ Koma nyama yakuthengo ya ku Lebanoni inadutsa pamenepo n’kupondaponda chitsamba chaminga chija.+
-
-
Yesaya 37:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Kudzera mwa antchito ako watonza Yehova ndipo wanena kuti,+
Ndi magaleta anga ankhondo ambiri, ine,+
Ineyo ndidzakwera ndithu madera amapiri mpaka pamwamba.+
Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni+
Ndipo ndidzadula mitengo yake ya mkungudza italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri yofanana ndi mkungudza.+
Ndidzalowa kumalo ake okhala akutali kwambiri, kunkhalango yokongola.+
-