Deuteronomo 28:48 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 48 Udzatumikira adani ako+ amene Yehova adzawatuma kuti akuukire. Udzawatumikira uli ndi njala,+ ludzu, usiwa ndiponso ukusowa china chilichonse. Adzakuveka goli lachitsulo m’khosi lako kufikira atakufafaniza.+ Oweruza 4:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Choncho Yehova anawagulitsa+ kwa Yabini mfumu yachikanani, imene inali kulamulira ku Hazori.+ Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Sisera,+ yemwe anali kukhala ku Haroseti-ha-goimu.+ Salimo 44:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Mwagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika kwambiri,+Ndipo simunapeze phindu ndi mtengo wawo.
48 Udzatumikira adani ako+ amene Yehova adzawatuma kuti akuukire. Udzawatumikira uli ndi njala,+ ludzu, usiwa ndiponso ukusowa china chilichonse. Adzakuveka goli lachitsulo m’khosi lako kufikira atakufafaniza.+
2 Choncho Yehova anawagulitsa+ kwa Yabini mfumu yachikanani, imene inali kulamulira ku Hazori.+ Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Sisera,+ yemwe anali kukhala ku Haroseti-ha-goimu.+