Genesis 45:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Aliyense wa iwo anam’patsa chovala choti asinthire,+ koma Benjamini anam’patsa zovala zosinthira zisanu, ndi ndalama zasiliva 300.+ Oweruza 14:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Pamenepo mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye.+ Choncho anapita ku Asikeloni+ kumene anakapha amuna 30, ndipo anatenga zovala zawo n’kuzipereka kwa amene anamasulira mwambi aja.+ Koma mkwiyo wake unapitiriza kuyaka, ndipo anapita kunyumba ya bambo ake. 2 Mafumu 5:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ndiyeno mfumu ya Siriya inauza Namani kuti: “Nyamuka, ndikupatsa kalata upite kwa mfumu ya Isiraeli.” Choncho iye ananyamuka atatenga+ matalente* 10 a siliva, masekeli 6,000 a golide,+ ndi zovala 10.+ 2 Mafumu 5:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Gehazi anayankha kuti: “Inde n’kwabwino. Mbuyanga+ wandituma+ kuti, ‘Posachedwapa kwabwera anyamata awiri, ana a aneneri,+ kuchokera kudera lamapiri la Efuraimu. Muwapatseko talente imodzi ya siliva ndi zovala ziwiri.’”+
22 Aliyense wa iwo anam’patsa chovala choti asinthire,+ koma Benjamini anam’patsa zovala zosinthira zisanu, ndi ndalama zasiliva 300.+
19 Pamenepo mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa iye.+ Choncho anapita ku Asikeloni+ kumene anakapha amuna 30, ndipo anatenga zovala zawo n’kuzipereka kwa amene anamasulira mwambi aja.+ Koma mkwiyo wake unapitiriza kuyaka, ndipo anapita kunyumba ya bambo ake.
5 Ndiyeno mfumu ya Siriya inauza Namani kuti: “Nyamuka, ndikupatsa kalata upite kwa mfumu ya Isiraeli.” Choncho iye ananyamuka atatenga+ matalente* 10 a siliva, masekeli 6,000 a golide,+ ndi zovala 10.+
22 Gehazi anayankha kuti: “Inde n’kwabwino. Mbuyanga+ wandituma+ kuti, ‘Posachedwapa kwabwera anyamata awiri, ana a aneneri,+ kuchokera kudera lamapiri la Efuraimu. Muwapatseko talente imodzi ya siliva ndi zovala ziwiri.’”+