Numeri 13:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Powatumiza kuti akazonde dziko la Kanani, Mose anawauza kuti: “Pitani ku Negebu,+ ndipo mukafike kudera lamapiri.+ Yoswa 2:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Tsopano Yoswa mwana wa Nuni anatumiza amuna awiri mwachinsinsi monga azondi kuchokera ku Sitimu.+ Anawalangiza kuti: “Pitani, mukazonde dzikolo ndi mzinda wa Yeriko.” Chotero iwo anapita n’kukafika kunyumba ya mayi wina yemwe anali hule, dzina lake Rahabi,+ n’kukhala kumeneko. Yoswa 7:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Tsopano Yoswa anatumiza amuna ena kuchokera ku Yeriko kupita ku Ai,+ pafupi ndi Beti-aveni,+ kum’mawa kwa Beteli.+ Iye anawauza kuti: “Pitani kumeneko, mukazonde dzikolo.” Amunawo anapita, n’kukazonda dziko la Ai.+ Oweruza 1:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Pamenepo a nyumba ya Yosefe anayamba kuchita ukazitape+ pamzinda wa Beteli (poyamba dzina la mzindawu linali Luzi).+ 1 Samueli 26:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Choncho Davide anatumiza azondi+ kuti akaone ngati Sauli wabweradi.
17 Powatumiza kuti akazonde dziko la Kanani, Mose anawauza kuti: “Pitani ku Negebu,+ ndipo mukafike kudera lamapiri.+
2 Tsopano Yoswa mwana wa Nuni anatumiza amuna awiri mwachinsinsi monga azondi kuchokera ku Sitimu.+ Anawalangiza kuti: “Pitani, mukazonde dzikolo ndi mzinda wa Yeriko.” Chotero iwo anapita n’kukafika kunyumba ya mayi wina yemwe anali hule, dzina lake Rahabi,+ n’kukhala kumeneko.
2 Tsopano Yoswa anatumiza amuna ena kuchokera ku Yeriko kupita ku Ai,+ pafupi ndi Beti-aveni,+ kum’mawa kwa Beteli.+ Iye anawauza kuti: “Pitani kumeneko, mukazonde dzikolo.” Amunawo anapita, n’kukazonda dziko la Ai.+
23 Pamenepo a nyumba ya Yosefe anayamba kuchita ukazitape+ pamzinda wa Beteli (poyamba dzina la mzindawu linali Luzi).+