Levitiko 25:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 “‘M’bale wanu akasauka n’kugulitsa ena mwa malo ake, wowombola amene ndi wachibale wake wapafupi azibwera ndi kugulanso zimene m’bale wakeyo anagulitsa.+ Deuteronomo 25:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 “Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi n’kumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mlendo wochokera m’banja lina. Mlamu wake apite kwa iye ndi kum’tenga kukhala mkazi wake, ndipo achite ukwati wa pachilamu.+ Rute 3:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pamenepo anafunsa kuti: “Ndiwe yani?” Poyankha, Rute anati: “Ndine Rute kapolo wanu. Mufunditse kapolo wanu chovala chanu, pakuti ndinu wotiwombola.”+ Rute 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Komano ngakhale kuti ndinedi wokuwombolani,+ pali wachibale wina wapafupi kwambiri kuposa ine+ amene angakuwombole. Aefeso 1:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Kudzera mwa iyeyu, tinamasulidwa ndi dipo* la magazi+ ake, inde, takhululukidwa+ machimo athu, malinga ndi chuma cha kukoma mtima kwake kwakukulu.+ Aheberi 2:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Chotero, popeza kuti “ana” amenewo onse ndi amagazi ndi mnofu, iyenso anakhala wamagazi ndi mnofu.+ Anachita izi kuti kudzera mu imfa yake,+ awononge+ Mdyerekezi,+ amene ali ndi njira yobweretsera imfa.+
25 “‘M’bale wanu akasauka n’kugulitsa ena mwa malo ake, wowombola amene ndi wachibale wake wapafupi azibwera ndi kugulanso zimene m’bale wakeyo anagulitsa.+
5 “Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi n’kumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mlendo wochokera m’banja lina. Mlamu wake apite kwa iye ndi kum’tenga kukhala mkazi wake, ndipo achite ukwati wa pachilamu.+
9 Pamenepo anafunsa kuti: “Ndiwe yani?” Poyankha, Rute anati: “Ndine Rute kapolo wanu. Mufunditse kapolo wanu chovala chanu, pakuti ndinu wotiwombola.”+
12 Komano ngakhale kuti ndinedi wokuwombolani,+ pali wachibale wina wapafupi kwambiri kuposa ine+ amene angakuwombole.
7 Kudzera mwa iyeyu, tinamasulidwa ndi dipo* la magazi+ ake, inde, takhululukidwa+ machimo athu, malinga ndi chuma cha kukoma mtima kwake kwakukulu.+
14 Chotero, popeza kuti “ana” amenewo onse ndi amagazi ndi mnofu, iyenso anakhala wamagazi ndi mnofu.+ Anachita izi kuti kudzera mu imfa yake,+ awononge+ Mdyerekezi,+ amene ali ndi njira yobweretsera imfa.+