Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+

      Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+

      Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+

      Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+

  • Salimo 94:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 94 Inu Yehova, Mulungu wobwezera anthu oipa,+

      Inu Mulungu wobwezera anthu oipa, walani!+

  • Nahumu 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.+ Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi waukali.+ Yehova amabwezera adani ake+ ndipo saiwala zoipa zimene iwo anachita.+

  • Aroma 12:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Okondedwa, musabwezere choipa,+ koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.+ Pakuti Malemba amati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.”+

  • Aheberi 10:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Pakuti timamudziwa amene anati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzabwezera ndine.”+ Ndiponso: “Yehova adzaweruza anthu ake.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena