Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+

      Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+

      Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+

      Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+

  • Yesaya 35:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Amene ali ndi nkhawa mumtima mwawo muwauze kuti:+ “Limbani mtima.+ Musachite mantha.+ Pakuti Mulungu wanu adzabwera n’kudzabwezera adani anu.+ Mulungu adzabwezera chilango.+ Iye adzabwera n’kukupulumutsani.”+

  • Yeremiya 50:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 “Kukumveka phokoso la anthu amene akuthawa komanso amene apulumuka m’dziko la Babulo+ kuti akanene ku Ziyoni za chilango chimene Yehova Mulungu wathu akubwezera.+ Iye akubwezera kuwonongedwa kwa kachisi wake.+

  • Nahumu 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.+ Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi waukali.+ Yehova amabwezera adani ake+ ndipo saiwala zoipa zimene iwo anachita.+

  • Aroma 12:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Okondedwa, musabwezere choipa,+ koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.+ Pakuti Malemba amati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.”+

  • 1 Atesalonika 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Koma akufuna kuti pasapezeke wina wopweteka m’bale wake kapena womuphwanyira ufulu wake pa nkhani imeneyi,+ chifukwa Yehova adzalanga anthu onse ochita zimenezi,+ monga mmene tinakuuzirani kale ndi kukufotokozerani momveka bwino.+

  • 2 Atesalonika 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Chiweruzo cha Mulunguchi n’cholungama chifukwa akubwezera masautso kwa amene amakusautsani.+

  • Aheberi 10:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Pakuti timamudziwa amene anati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzabwezera ndine.”+ Ndiponso: “Yehova adzaweruza anthu ake.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena