28 Zitatero, Samueli anamuuza kuti: “Yehova wang’amba+ ndi kuchotsa ufumu wa Isiraeli kwa iwe lero, ndipo adzaupereka kwa mnzako, munthu woyenerera kuposa iwe.+
5 inenso ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu mu ufumu wa Isiraeli mpaka kalekale, monga momwe ndinalonjezera Davide bambo ako kuti, ‘Munthu wa m’banja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+