27 Pakuti inu Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, mwaululira ine mtumiki wanu kuti, ‘Ndidzakumangira nyumba.’*+ N’chifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera kwa inu pemphero lino.+
10 Iyeyo ndi amene adzamanga nyumba ya dzina langa.+ Adzakhala mwana+ wanga, ndipo ine ndidzakhala atate wake.+ Ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu+ pa Isiraeli ndipo sudzagwedezeka mpaka kalekale.’