4 Komanso kuti Yehova adzakwaniritse mawu ake okhudza ine amene analankhula,+ akuti, ‘Ana ako+ akadzasamalira njira zawo, mwa kuyenda+ mokhulupirika+ pamaso panga ndi mtima wawo wonse+ ndi moyo wawo wonse, munthu wa m’banja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+