Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 28:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 “Koma iwe patula Aroni m’bale wako pamodzi ndi ana ake pakati pa ana a Isiraeli, ndipo Aroniyo+ atumikire monga wansembe wanga pamodzi ndi ana akewo,+ Nadabu, Abihu,+ Eleazara ndi Itamara.+

  • Ekisodo 39:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Ndiyeno anapanga zovala+ zosokedwa bwino zoti azivala potumikira m’malo oyera,+ pogwiritsa ntchito ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi ulusi wofiira kwambiri.+ Motero anapanga zovala zopatulika+ za Aroni, monga mmene Yehova analamulira Mose.

  • Levitiko 8:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pomalizira, Mose anathira ena mwa mafuta odzozera pamutu pa Aroni ndi kum’dzoza kuti akhale wopatulika.+

  • Numeri 16:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ndiyeno Mose analankhula ndi Kora ndiponso khamu lonselo, kuti: “Mawa m’mawa, Yehova aonetsa amene ali wake+ ndiponso amene ali woyera.+ Aonetsa amene ayenera kuima pamaso pake,+ ndipo amene ati am’sankheyo+ adzaima pamaso pake.

  • Numeri 17:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Chimene chichitike n’chakuti, munthu amene ndimusankheyo,+ ndodo yake idzaphuka, ndipo ndidzathetseratu kudandaula+ kwa ana a Isiraeli kumene akuchita motsutsana ndi ine, pamene akudandaula motsutsana nawe.”+

  • Numeri 17:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Tsiku lotsatira, Mose atalowa m’chihema cha Umbonicho, anangoona kuti ndodo ya Aroni ya nyumba ya Levi inali itaphuka. Ndodoyo inali itaphuka ndipo inali kumasula maluwa ndi kubala zipatso za amondi zakupsa.

  • Salimo 99:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Mose ndi Aroni anali pakati pa ansembe ake,+

      Samueli anali pakati pa anthu amene anali kuitana pa dzina lake.+

      Iwo anali kuitana Yehova, ndipo iye anali kuwayankha.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena