1 Samueli 28:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Tsopano Samueli anali atamwalira ndipo Aisiraeli anali atamulira ndi kumuika m’manda mumzinda wakwawo ku Rama.+ Ndipo Sauli anali atachotsa anthu olankhula ndi mizimu ndi akatswiri olosera zam’tsogolo m’dzikolo.+ Salimo 146:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+ Mlaliki 9:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse.+ Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika.+ 2 Akorinto 4:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Pakati pa anthu amenewa, mulungu wa nthawi* ino+ wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira,+ kuti asaone+ kuwala+ kwa uthenga wabwino waulemerero+ wonena za Khristu, yemwe ali chifaniziro+ cha Mulungu. 2 Akorinto 11:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndipo zimenezo n’zosadabwitsa, popeza ngakhale Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala.+
3 Tsopano Samueli anali atamwalira ndipo Aisiraeli anali atamulira ndi kumuika m’manda mumzinda wakwawo ku Rama.+ Ndipo Sauli anali atachotsa anthu olankhula ndi mizimu ndi akatswiri olosera zam’tsogolo m’dzikolo.+
4 Mzimu* wake umachoka,+ ndipo iye amabwerera kunthaka.+Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.+
5 Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse.+ Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika.+
4 Pakati pa anthu amenewa, mulungu wa nthawi* ino+ wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira,+ kuti asaone+ kuwala+ kwa uthenga wabwino waulemerero+ wonena za Khristu, yemwe ali chifaniziro+ cha Mulungu.