2 Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka ndi kupita ku Baale-yuda+ kuti akatenge likasa+ la Mulungu woona. Pa likasa limeneli amaitanira dzina+ la Yehova wa makamu,+ wokhala pamwamba pa akerubi.+
5 Chotero, Davide anasonkhanitsa+ Aisiraeli onse kuchokera kumtsinje wa Iguputo+ mpaka kukafika polowera ku Hamati,+ kuti akatenge likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu.+