Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 6:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma iye anayankha kuti: “Pepani Yehova. Kodi Isiraeli ndidzam’pulumutsa ndi chiyani?+ Pajatu banja lathu* ndilo laling’ono zedi m’fuko lonse la Manase, ndipo m’nyumba ya bambo anga, wamng’ono kwambiri ndine.”+

  • Miyambo 3:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Onyoza,+ iye amawanyoza,+ koma ofatsa amawakomera mtima.+

  • Miyambo 11:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Kodi kudzikweza kwafika? Ndiye kuti manyazinso afika.+ Koma nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.+

  • Miyambo 18:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Munthu asanagwe, mtima wake umadzikweza,+ ndipo asanapeze ulemerero, amadzichepetsa.+

  • Miyambo 22:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Zotsatirapo za kudzichepetsa ndiponso kuopa Yehova ndizo chuma, ulemerero, ndi moyo.+

  • Luka 14:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pakuti aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”+

  • Yakobo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+

  • 1 Petulo 5:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Chimodzimodzinso inu anyamata. Muzigonjera+ amuna achikulire. Koma nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa,+ chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena