-
1 Samueli 18:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Davide pamodzi ndi asilikali ake ananyamuka, ndipo anakapha+ amuna 200 achifilisiti. Ndiyeno Davide anabwerako atatenga makungu awo a kunsonga,+ ndipo makungu onsewo anawapereka kwa mfumu kuti achite naye mgwirizano wa ukwati. Pamenepo Sauli anapereka Mikala, mwana wake wamkazi, kwa Davide kuti akhale mkazi wake.+
-
-
2 Samueli 6:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Tsopano Davide anabwerera kunyumba kwake kuti akadalitse banja lake.+ Pamenepo Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kukakumana naye ndipo anati: “Lerotu mfumu ya Isiraeli yaonetsa ulemerero wake+ mwa kudzivula pamaso pa akapolo aakazi a atumiki ake, monga mmene munthu wopanda nzeru amadzivulira mopanda manyazi ngakhale pang’ono!”+
-