Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 18:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Tsopano Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anali kukonda Davide, ndipo anthu anauza Sauli zimenezi. Sauli atamva nkhani imeneyi anasangalala.

  • 1 Samueli 18:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Davide pamodzi ndi asilikali ake ananyamuka, ndipo anakapha+ amuna 200 achifilisiti. Ndiyeno Davide anabwerako atatenga makungu awo a kunsonga,+ ndipo makungu onsewo anawapereka kwa mfumu kuti achite naye mgwirizano wa ukwati. Pamenepo Sauli anapereka Mikala, mwana wake wamkazi, kwa Davide kuti akhale mkazi wake.+

  • 1 Samueli 19:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Kenako Sauli anatumiza amithenga+ kunyumba ya Davide kuti akaizungulire ndi kupha Davide m’mawa mwa tsiku limenelo.+ Koma Mikala mkazi wa Davide anauza Davideyo kuti: “Ngati supulumutsa moyo wako usiku uno, mawa ukhala utaphedwa.”

  • 1 Samueli 25:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Koma Sauli anali atapereka Mikala+ mwana wake wamkazi, mkazi wake wa Davide, kwa Paliti,+ mwana wamwamuna wa Laisi wa ku Galimu.+

  • 1 Mbiri 15:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ndiyeno likasa la pangano+ la Yehova litafika mu Mzinda wa Davide, Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pawindo kuyang’ana pansi, ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha ndi kusangalala.+ Pamenepo Mikala anayamba kum’peputsa+ mumtima mwake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena