26 Ndiyeno Davide anayamba kufunsa amuna amene anali ataimirira pafupi naye kuti: “Kodi munthu amene angakaphe Mfilisiti+ ameneyu ndi kuchotsa chitonzo pa Isiraeli+ amuchitira chiyani? Kodi Mfilisiti wosadulidwa+ ameneyu ndani kuti azinyoza+ asilikali a Mulungu wamoyo?”+