13 Dzuka! Yeretsa anthuwa,+ uwauze kuti, ‘Mawa mudziyeretse, pakuti Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Kalanga Isiraeli, pakati panu pali zinthu zoyenera kuwonongedwa.+ Anthu inu simudzathanso kulimbana ndi adani anu, kufikira mutachotsa pakati panu zinthu zoyenera kuwonongedwazo.