19 Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a mu Yuda anamupha? Kodi iye sanaope Yehova ndi kukhazika pansi mtima wa Yehova?+ Kodi atatero, Yehova sanasinthe maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti adzawagwetsera?+ Pamenepatu ife tikudziitanira tsoka lalikulu.+
13 Ng’ambani mitima yanu+ osati zovala zanu+ ndipo bwererani kwa Yehova Mulungu wanu pakuti iye ndi wachisomo, wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+ Ndithu, iye adzakumverani chisoni chifukwa cha tsokalo.+