26 Ndiyeno Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamalopo,+ ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Komanso anaitana pa dzina la Yehova+ yemwe tsopano anamuyankha ndi moto+ wochokera kumwamba umene unafika paguwa lansembe yopsereza.