1 Mbiri 15:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Davide anapitiriza kumanga nyumba+ zake mu Mzinda wa Davide, ndipo anakonza malo+ oikapo likasa la Mulungu woona, n’kulimangira hema. 1 Mbiri 16:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Motero analowetsa+ likasa la Mulungu woona muhema limene Davide anamanga, n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu woona.+ 2 Mbiri 1:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Koma Davide anali atachotsa likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu+ n’kukaliika kumalo amene iye anakonza,+ pakuti anali atamanga hema wa likasalo ku Yerusalemu.+
15 Davide anapitiriza kumanga nyumba+ zake mu Mzinda wa Davide, ndipo anakonza malo+ oikapo likasa la Mulungu woona, n’kulimangira hema.
16 Motero analowetsa+ likasa la Mulungu woona muhema limene Davide anamanga, n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu woona.+
4 Koma Davide anali atachotsa likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu+ n’kukaliika kumalo amene iye anakonza,+ pakuti anali atamanga hema wa likasalo ku Yerusalemu.+