8 Pa nthawi imeneyo Solomo+ anauza akulu,+ mitu yonse ya mafuko,+ ndi atsogoleri a makolo+ a ana a Isiraeli, kuti asonkhane+ kwa Mfumu Solomo ku Yerusalemu. Anawauza kuti akatenge likasa la pangano+ la Yehova ku Mzinda wa Davide,+ kutanthauza Ziyoni.+