Ekisodo 40:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Pamene Mose anali kuutsa chihema chopatulikacho, anayala pansi zitsulo zake zamphako+ ndi kukhazikapo mafelemu.+ Ndiyeno analowetsa mitengo yake yonyamulira+ ndi kuimika mizati pamalo ake.+ Ekisodo 40:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Pamenepo mtambo+ unayamba kuphimba chihema chokumanako, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza m’chihemacho. 1 Mbiri 17:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa Isiraeli mu Iguputo kufikira lero,+ sindinakhalepo m’nyumba, koma ndakhala m’hema ndi m’hema ndiponso m’chihema chopatulika+ ndi m’chihema chopatulika.+ Machitidwe 7:44 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 44 “Makolo athuwo anali ndi chihema cha umboni m’chipululu. Anachipanga potsatira malangizo amene Mulungu anapereka pamene anali kulankhula ndi Mose. Mulungu anauza Mose kuti apange chihemacho molingana ndi chithunzi chimene anachiona.+
18 Pamene Mose anali kuutsa chihema chopatulikacho, anayala pansi zitsulo zake zamphako+ ndi kukhazikapo mafelemu.+ Ndiyeno analowetsa mitengo yake yonyamulira+ ndi kuimika mizati pamalo ake.+
34 Pamenepo mtambo+ unayamba kuphimba chihema chokumanako, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza m’chihemacho.
5 Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa Isiraeli mu Iguputo kufikira lero,+ sindinakhalepo m’nyumba, koma ndakhala m’hema ndi m’hema ndiponso m’chihema chopatulika+ ndi m’chihema chopatulika.+
44 “Makolo athuwo anali ndi chihema cha umboni m’chipululu. Anachipanga potsatira malangizo amene Mulungu anapereka pamene anali kulankhula ndi Mose. Mulungu anauza Mose kuti apange chihemacho molingana ndi chithunzi chimene anachiona.+