18 Choncho pa tsiku la 7, Samisoni asanalowe m’chipinda cha mkaziyo,+ amuna a mumzindawo anamuuza kuti:
“Kodi chokoma kuposa uchi n’chiyani,
Ndipo champhamvu kuposa mkango n’chiyani?”+
Poyankha iye anawauza kuti:
“Mukanapanda kulima ndi ng’ombe yanga yaikazi,+
Simukanatha kumasulira mwambi wanga.”+