7 “Ngati mwamunayo sakufuna kutenga mkazi wamasiye wa m’bale wakeyo, mkaziyo azinyamuka ndi kupita kuchipata kwa akulu+ ndi kuwauza kuti, ‘M’bale wa mwamuna wanga wakana kusunga dzina la m’bale wake mu Isiraeli. Sanavomereze kuchita ukwati wa pachilamu ndi ine.’