4 Koma mfumu ya Asuri inaona kuti Hoshiya anali kuichitira chiwembu,+ chifukwa chakuti iye anatumiza amithenga kwa So mfumu ya Iguputo,+ ndiponso sanapereke msonkho kwa mfumu ya Asuri monga anali kuchitira zaka zam’mbuyo. Choncho mfumu ya Asuri inam’manga n’kumutsekera m’ndende.+