-
2 Samueli 20:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Patapita nthawi, Davide anafika kunyumba yake ku Yerusalemu.+ Ndiyeno mfumuyo inatenga akazi 10+ aja, adzakazi amene anawasiya kuti azisamalira nyumba yake, ndipo anawatsekera m’nyumba ina koma anapitiriza kuwapatsa chakudya. Iye sanagone nawonso,+ koma anawatsekerabe kufikira tsiku la kufa kwawo. Iwo anakhala akazi amasiye mwamuna wawo ali moyo.
-