27 Abineri atabwerera ku Heburoni,+ Yowabu anam’tengera pambali kuchipata kuti alankhulane naye pa awiri.+ Koma kumeneko anamubaya pamimba+ moti anafa chifukwa chokhetsa magazi a Asaheli,+ m’bale wake wa Yowabu.
7 Mtsogoleri wachinayi, wa mwezi wachinayi, anali Asaheli+ m’bale wake wa Yowabu,+ ndipo mwana wake Zebadiya anabwera pambuyo pake. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.