1 Mafumu 2:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Kenako Davide anagona limodzi ndi makolo ake,+ ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.+ 2 Mbiri 21:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Yehoramu anali ndi zaka 32 pamene anayamba kulamulira ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8. Pomalizira pake iye anapita popanda womumvera chisoni.+ Choncho anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide,+ koma osati m’manda a mafumu.+
20 Yehoramu anali ndi zaka 32 pamene anayamba kulamulira ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 8. Pomalizira pake iye anapita popanda womumvera chisoni.+ Choncho anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide,+ koma osati m’manda a mafumu.+