Ekisodo 10:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Chotero ndikhululukireni+ tchimo langa kamodzi kokha kano, ndipo chondererani+ Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wakuphawu.” Numeri 21:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Anthuwo ataona zimenezo, anapita kwa Mose n’kumuuza kuti: “Tachimwa ife,+ chifukwa talankhula mowiringula kwa Yehova ndiponso kwa inuyo. Tipepesereni kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.”+ Pamenepo Mose anayamba kuwapepesera kwa Mulungu.+ Yeremiya 37:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Mfumu Zedekiya inatumiza Yehukali+ mwana wa Selemiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya+ wansembe kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga wakuti: “Chonde, tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu.”+ Machitidwe 8:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Poyankha Simoni uja anati: “Amuna inu, ndipemphereni chonde kwa Yehova mopembedzera+ kuti zonse mwanenazo zisandigwere.” Yakobo 5:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Choncho muululirane machimo anu poyera+ ndi kupemphererana, kuti muchiritsidwe.+ Pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.+
17 Chotero ndikhululukireni+ tchimo langa kamodzi kokha kano, ndipo chondererani+ Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wakuphawu.”
7 Anthuwo ataona zimenezo, anapita kwa Mose n’kumuuza kuti: “Tachimwa ife,+ chifukwa talankhula mowiringula kwa Yehova ndiponso kwa inuyo. Tipepesereni kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.”+ Pamenepo Mose anayamba kuwapepesera kwa Mulungu.+
3 Mfumu Zedekiya inatumiza Yehukali+ mwana wa Selemiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya+ wansembe kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga wakuti: “Chonde, tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu.”+
24 Poyankha Simoni uja anati: “Amuna inu, ndipemphereni chonde kwa Yehova mopembedzera+ kuti zonse mwanenazo zisandigwere.”
16 Choncho muululirane machimo anu poyera+ ndi kupemphererana, kuti muchiritsidwe.+ Pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.+