19 Chotero Mulungu anang’amba nthaka ku Lehi ndipo madzi+ anayamba kutuluka panthakapo. Pamenepo Samisoni anamwa madziwo, moti anapezanso mphamvu+ ndi kutsitsimulidwa.+ N’chifukwa chake anatcha malowo kuti Eni-hakore. Malo amenewa ali ku Lehi kufikira lero.