1 Samueli 14:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kenako anthu amene anali kutchire mumsasa ndi anthu onse kumudzi wa asilikaliwo anayamba kunjenjemera.+ Anthu olanda katundu+ nawonso anali kunjenjemera, ndipo nthaka inayamba kugwedezeka.+ Zimenezi zinali zochokera kwa Mulungu.+ Yobu 9:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Amachititsa dziko lapansi kunjenjemera pamalo ake,Mwakuti zipilala+ zake zimagwedezeka. Salimo 68:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Dziko lapansi linagwedezeka,+Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,+Phiri ili la Sinai linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu,+ Mulungu wa Isiraeli.+ Nahumu 1:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Mapiri agwedezeka chifukwa cha iye ndipo zitunda zasungunuka.+ Dziko lapansi, nthaka ndi zinthu zonse zokhala m’dzikomo zidzanjenjemera.+
15 Kenako anthu amene anali kutchire mumsasa ndi anthu onse kumudzi wa asilikaliwo anayamba kunjenjemera.+ Anthu olanda katundu+ nawonso anali kunjenjemera, ndipo nthaka inayamba kugwedezeka.+ Zimenezi zinali zochokera kwa Mulungu.+
8 Dziko lapansi linagwedezeka,+Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,+Phiri ili la Sinai linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu,+ Mulungu wa Isiraeli.+
5 Mapiri agwedezeka chifukwa cha iye ndipo zitunda zasungunuka.+ Dziko lapansi, nthaka ndi zinthu zonse zokhala m’dzikomo zidzanjenjemera.+