17 Kenako Elisa anati: “Tsegulani windo lakum’mawa.” Iye analitsegula. Ndiyeno Elisa anati: “Ponyani muviwo!” Choncho iye anauponya. Tsopano Elisa anati: “Muvi wa Yehova wopulumutsa! Muvi wopulumutsa+ kwa Asiriya! Ndithu mudzapha Asiriya ku Afeki+ mpaka kuwamaliza.”