1 Samueli
29 Ndiyeno Afilisiti+ anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, pamene Aisiraeli anamanga msasa pafupi ndi kasupe amene anali ku Yezereeli.+ 2 Olamulira ogwirizana+ a Afilisiti anali kudutsa m’magulu a asilikali 100, ndi 1,000, ndipo Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anadutsa pambuyo pawo limodzi ndi Akisi.+ 3 Ndiyeno akalonga a Afilisiti anayamba kunena kuti: “Kodi Aheberi+ awa akufuna chiyani kuno?” Pamenepo Akisi anayankha akalonga a Afilisitiwo kuti: “Kodi uyu si Davide, mtumiki wa Sauli, mfumu ya Isiraeli? Iyetu wakhala ndi ine kuno kwa chaka chimodzi kapena ziwiri,+ ndipo kuyambira tsiku limene anathawira kwa ine kufikira lero, sindinam’peze+ ndi chifukwa ngakhale chimodzi.” 4 Pamenepo akalonga a Afilisiti anam’psera mtima kwambiri Akisi, ndipo anati: “Muuze abwerere,+ apite kumalo amene unam’patsa. Usamulole kuti apite nafe kunkhondo chifukwa angakatitembenukire+ kumeneko. Ukuganiza kuti munthu ameneyu adzakometsera dzina lake ndi chiyani kwa mbuye wake? Si mitu ya asilikali athu kodi? 5 Kodi uyu si Davide uja amene ankamuimbira nyimbo molandizana mawu, akuvina n’kumati, ‘Sauli wakantha adani ake masauzande, ndipo Davide wakantha masauzande makumimakumi’?”+
6 Choncho Akisi+ anaitana Davide ndi kumuuza kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ iweyo ndiwe wowongoka mtima, ndipo ndasangalala+ kuti wabwera nane+ kunkhondo, pakuti sindinapeze choipa chilichonse mwa iwe kuyambira tsiku limene unabwera kwa ine kufikira lero.+ Koma olamulira ogwirizana+ sakukuona bwino. 7 Choncho, bwerera mwamtendere, kuti usachite chilichonse chimene olamulira ogwirizana a Afilisiti angachione kukhala choipa.” 8 Koma Davide anayankha Akisi kuti: “Ndibwerere chifukwa chiyani? Ndalakwa chiyani,+ ndipo mwapeza chiyani mwa ine mtumiki wanu kuchokera pa tsiku limene ndinabwera kudzakhala nanu kufikira lero,+ kuti ndisapite kukamenyana ndi adani anu mbuyanga mfumu?” 9 Pamenepo Akisi anayankha Davide kuti: “Ndikudziwa bwino kuti wakhala ukundichitira zinthu zabwino, ngati mngelo wa Mulungu.+ Koma akalonga a Afilisiti ndi amene anena kuti, ‘Musalole kuti ameneyu apite nafe kunkhondo.’ 10 Choncho udzuke m’mawa kwambiri pamodzi ndi atumiki a mbuye wako amene anabwera nawe pamodzi. Mukangoona kuti kwayera mudzuke ndi kunyamuka.”+
11 Chotero Davide anadzuka m’mawa kwambiri+ pamodzi ndi amuna amene anali kuyenda naye ndi kubwerera kudziko la Afilisiti m’mawa umenewo. Koma Afilisitiwo anapita ku Yezereeli.+