20 Choncho Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a gulu lake lankhondo kuti akamenyane ndi mizinda ya Isiraeli. Iwo anawononga mizinda ya Iyoni,+ Dani,+ Abele-beti-maaka,+ ndi Kinereti yense mpaka dziko lonse la Nafitali.+
4 Choncho Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a gulu lake lankhondo kuti akamenyane ndi mizinda ya Isiraeli. Iwo anawononga Iyoni,+ Dani,+ Abele-maimu,+ ndi malo onse osungiramo zinthu+ a m’mizinda ya Nafitali.+