22 Mfumu Solomo itamva zimenezi inafunsa mayi ake kuti: “N’chifukwa chiyani mukum’pemphera Adoniyayu Abisagi Msunemu? M’pemphereninso ufumu+ (chifukwa iye ndi mkulu wanga).+ Mupemphereni ufumu Adoniyayo. Mupempherenso wansembe Abiyatara+ ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya.”+