Ekisodo 14:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Iye anali kugulula mawilo a magaleta awo moti anali kuwayendetsa movutikira.+ Pamenepo Aiguputo anayamba kunena kuti: “Tiyeni tithawe pamaso pa Isiraeli, chifukwa Yehova akuwamenyera nkhondo yolimbana ndi Aiguputo.”+ Yesaya 5:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Mivi yawo ndi yakuthwa ndipo mauta awo onse ndi okungika.+ Ziboda za mahatchi awo n’zolimba ngati mwala wa nsangalabwi.+ Mawilo a magaleta awo ali ngati mphepo yamkuntho.+ Yesaya 28:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Pakuti anthu sapuntha chitowe chakuda ndi chida chopunthira+ ndipo pachitowe chamtundu wina sayendetsapo mawilo a ngolo yopunthira mbewu. Nthawi zambiri chitowe chakuda amachipuntha ndi ndodo+ ndipo chitowe chamtundu wina amachipuntha ndi kamtengo.
25 Iye anali kugulula mawilo a magaleta awo moti anali kuwayendetsa movutikira.+ Pamenepo Aiguputo anayamba kunena kuti: “Tiyeni tithawe pamaso pa Isiraeli, chifukwa Yehova akuwamenyera nkhondo yolimbana ndi Aiguputo.”+
28 Mivi yawo ndi yakuthwa ndipo mauta awo onse ndi okungika.+ Ziboda za mahatchi awo n’zolimba ngati mwala wa nsangalabwi.+ Mawilo a magaleta awo ali ngati mphepo yamkuntho.+
27 Pakuti anthu sapuntha chitowe chakuda ndi chida chopunthira+ ndipo pachitowe chamtundu wina sayendetsapo mawilo a ngolo yopunthira mbewu. Nthawi zambiri chitowe chakuda amachipuntha ndi ndodo+ ndipo chitowe chamtundu wina amachipuntha ndi kamtengo.