8 Choncho Davide pa tsiku limenelo anati: “Aliyense wofuna kukaukira Ayebusi+ adutse m’ngalande zamadzi+ ndi kukakumana ndi anthu olumala ndi akhungu, anthu amene ine Davide ndimadana nawo kwambiri!” N’chifukwa chake pali mawu onena kuti: “Wakhungu ndi wolumala asalowe m’nyumba.”