49 Panali pa nthawi imeneyo pamene Ahaziya mwana wa Ahabu anapempha Yehosafati kuti: “Bwanji antchito anga apite pamodzi ndi antchito anu m’zombozo?” Koma Yehosafati anakana.+
18 Hiramu,+ kudzera mwa antchito ake, ankatumizira Solomo zombo ndi antchito odziwa za panyanja.+ Iwo ankapita ku Ofiri+ pamodzi ndi antchito a Solomo kukatenga golide+ wokwana matalente* 450,+ ndipo anali kubwera naye kwa Mfumu Solomo.+