3 Kenako Solomo anachita mgwirizano wa ukwati+ ndi Farao mfumu ya Iguputo. Anatenga mwana wamkazi wa Faraoyo+ n’kubwera naye ku Mzinda wa Davide,+ kuti azikhala kaye kumeneko mpaka iye atamaliza kumanga nyumba yake,+ nyumba ya Yehova,+ ndi mpanda wozungulira Yerusalemu yense.+