8 Kenako Solomo anamanga nyumba yake yokhalamo kubwalo lina+ chapatali ndi nyumba ya Bwalo la Mpando Wachifumu. Kamangidwe ka nyumbayi kanali kofanana ndi ka Bwalo la Mpando Wachifumu. Panalinso nyumba ina yofanana ndi Bwaloli imene Solomo anamangira mwana wamkazi wa Farao+ amene iye anam’kwatira.
24 Mwana wamkazi wa Farao+ anachoka ku Mzinda wa Davide+ n’kukakhala kunyumba yake imene Solomo anam’mangira. Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamanga Chimulu cha Dothi.*+